TSIKU-LA-ADAMBO
SERMON TOPIC: TSIKU-LA-ADAMBO
Speaker: Gavin Paynter
Language: CHICHEWA
Date: 13 July 2017
Topic Groups:
Sermon synopsis: 1 Yohane 2:13 Ndikulemberani atate popeza mwamzindikira Iye, amene ali kuyambira pachiyambi.
Ndikulemberani anyamata popeza mwamulaka oyipayo, ndikulemberani ana popeza mwazindikira Atate.
Yohane analemba mosiyanitsa mitundu itatu ya akhristu:
1) Ana
2) Anyamata
3) Atate
Kodi kusiyana kwawo kuli pati?
1) Ana – Amasowa wina awayang’anire.
2) Anyamata – amadziyang’anira okha.
3) Atate – Samangodziyang’anira okha komanso amayang’aniranso anthu ena.
“Atate” ngakhalenso amayi sachita kubadwa, anyamata amakula kukhala abambo pamene atsikana amakula kukhala amayi. Izi adalankhula ndi bambo - David M. Gottesman
IP:Country:City:Region:
|