Sermon synopsis: Mateyu 5:7 “Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo. 8 Odala ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu. 9 Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu. 10 Odala ali akuzunzidwa chifukwa chachilungamo; chifukwa uli wao ufumu wakumwamba.
11 “Odala muli inu m’mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zirizonse chifukwa cha Ine. 12 Sekerani, sangalalani: Chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu kumwamba: Pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.”