Sermon synopsis: Mateyu analemba zizindikiro zodabwitsa zitatu zimene zinachitika tsiku limene Ambuye Yesu adapachikidwa.
1) Mdima pa dziko lonse la pansi.
2) Chinsalu chotchinga mkachisi chinang’ambika.
3) Chibvomerezi komanso chiukitso cha okhulupilira amene adafa kale.
Chifukwa chiyani Mulungu adapereka zizindikiro zimenezi?