ANTHU AKUGWIRA NTCHITO

SERMON TOPIC: ANTHU AKUGWIRA NTCHITO

Speaker: Gavin Paynter

Language: CHICHEWA

Date: 17 November 2013

Topic Groups:

Sermon synopsis: 2 Atesalonika 3:6 Ndipo tikulamulirani abale, m’dzina la Ambuye wathu, kuti mubwevuke kwa m’bale yense wakuyenda dwache dwache, osatsata mwambo umene anaulandila kwa ife. Pakuti mudziwa nokha m’mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhale dwache dwache mwa inu; kapena sitinadya mkate chabe padzanja lamunthu, komatu m’chivuto ndi m’chipsinjo tinagwira ntchito usiku ndi usana kuti tingalemetse inu. Sichifukwa tilibe ulamuliro komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu kuti mukatitsanze ife.
Pakutinso pamene tinali nanu tinakulamulirani ichi; Ngati munthu safuna kugwira ntchito asadyenso. Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwache dwache, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina. Koma oterewa tiwalamulira ndikuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete nadye chakudya cha iwo okha. Koma inu abale musaleme pakuchita zabwino. Koma ngati wina samvera mawu athu mkalata uyu, yang’anirani ameneyo, kuti musayanjane naye kuti achite manyazi. Koma musamuyese mdani, koma mumuyambilire ngati mbale.

- Download notes (1.92 MB, 2130 downloads)

- Download audio (9.37 MB, 1805 downloads)
- All sermons by Gavin Paynter

- All sermons in CHICHEWA




IP:Country:City:Region: