Doctrine of salvation - Part 1 - CHICHEWA

SERMON TOPIC: Doctrine of salvation - Part 1 - CHICHEWA

Speaker: Gavin Paynter

Language: CHICHEWA

Date: 17 July 2013

Topic Groups:

Sermon synopsis: Chikhristu chimati palibe ngakhale m’modzi angapulumutsidwe kudzera mu ntchito za iye yekha mu umunthu (kupanga miyambo, ntchito zabwino, kudzipatulira kuzinthu zina kapena kulingalira mozama).
Baibulo limaphunzitsa kuti munthu amabadwa mudziko lauchimo. Izi ndizotsatira za chikhalidwe chauchimo chomwe tidachitengera kuchokera kwa makolo athu oyamba. Choncho munthu ochimwa ndiye vuto osati yankho ku vuto la tchimo ayi.
Kukhulupilira kuti ungadzipulumutse wekha kuli ngati munthu womira m’madzi okhulupilira kuti angathe kudzivuula ndikudzikokera yekha kumtunda podzikoka ndevu zake zomwe. Munthuyu asoweka china chapadera monga thanthwe lolimba kapena bwato kuti akangamireko.
Munthu sangathe kudzipulumutsa yekha monganso momwe Chikho sichingadzithire chokha madzi kapena vinyo – apanso pasoweka china chake chapadera chothandizira.

- Download notes (1.43 MB, 1665 downloads)

- Download audio (7.16 MB, 1882 downloads)
- All sermons by Gavin Paynter

- All sermons in CHICHEWA




IP:Country:City:Region: